Bambo wa zaka 25, Foster Mathewe Saidi, wayamba kugwira ukayidi wa zaka 18 ku ndende kaamba komugona msungwana wa zaka zisanu ndi chimodzi.
M’neneri wa polisi ya Limbe mu mzinda wa Blanyre, Aubrey Singanyama, wati mkuluyu anapalamula mulanduwu pa 21 June chaka chino cha mma 8 koloko usiku pomwe ananyengerera msungwanayu pomukokera mnyumba mwake kuti akamupatse ndiwo zoti adyere nsima.
Mai ake a msungwanayu ndiwo anakatula nkhaniyi ku polisi atazindikira kuti mwana wawoyu wachitidwa chipongwechi ndipo izi zinadziwika atamufunsa kutsatira kuti msungwanayu amayenda movutika kusonyeza kuti amamva ululu kumalo ake obisika.
Senior Resident Magistrate Ackia Mwanyongo ndiye wapereka chigamulochi kwa Foster Mathewe Saidi. Saidi ndi wochokera m’mudzi mwa Mkawela mfumu yayikulu Inkosi Bvumbwe m’boma la Thyolo.
Pa nkhani yonga yomweyi, Senior Resident Magistrate Gift Msume wagamula kuti a Benjamin Hhlema a zaka 30, akagwire ukayidi ku ndende kwa zaka zitatu kaamba kogwilira msungwana wa zaka zisanu ndi zitatu ku Machinjiri mu mzinda wa Blantyre.