Boma la Tonse lalephera watero Mutharika

Mtsogoleri wakale wa dziko lino, yemwenso ndi mtsogoleri wa chipani cha Democratic Progressive (DPP), Arthur Peter Mutharika wati boma la Tonse lalephera kukwaniritsa zokhumba za a Malawi.

Kudzera pa tsamba lake la mchezo la Facebook, a Mutharika ati a Malawi akuvutika kupeza thandizo losiyanasiyana kuphatikizapo ziphaso zoyendera mwa zina.

Iwo ati mwa zina anthu akumagona pa mzere ku nthambi yoona zotukula ndi kulowa mdziko muno kudikira ziphaso zawo komanso umphawi wadzaoneneni womwe ulipo mdziko muno, zomwe ati sizidachitikepo chiyambileni ufulu wa demokalase mdziko muno.

Kuphatikiza apo a Mutharika ati chuma cha dziko lino nacho sichikuyenda bwino ponena kuti kwacha ikupitilira kuchepa mphamvu, mtengo wa katundu ukungokwera komanso ndalama ya kunja ikupitilira kusowa zomwenso zikukhudza anthu ochita malonda.

Komabe iwo ati anthu asataye chikhulupiliro ponena kuti kusintha kukubwera chaka cha mawa pomwe dziko lino likhale likuchititsa chisankho.

Mneneri wa boma la Tonse a Moses Kumkuyu sanayankhe lamya yawo titawaimbira kuti ayankhulepo pa nkhaniyi.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *