MCP sibwera ku msonkhano waukulu, yatero UDF

Chipani cha United Democratic (UDF) chatsimikiza kuti chasintha ganizo lake loyitana chipani cholamula cha Malawi Congress (MCP) kuti chidzakhale nawo pa mkumano waukulu wosankha atsogoleri a chipanichi pa 2 October mu mzinda wa Blantyre.

M’neneri wa chipani cha UDF, a Yusufu Mwawa, awuza YFM online kuti chipanichi chachita izi kutsatira pempho la gulu la otsatira chipanichi omwe anatemetsa nkhwangwa pa mwala kuti sakufuna kuti MCP izapezeke ku msonkhanowu.

“Ndi zowona kuti tagonjera zomwe masapota athu akufuna molingananso ndi demokalase,” anatero a Mwawa.

Iwo atinso wapampando wa komiti yoyendetsa msonkhano wawukulu wa chipanichi, a Aisha Mambo Adams, omwe zinamveka kuti anatula pansi udindo wawo kamba ka nkhaniyi, adakali pa udindowu.

“Ayi iwotu sanatule pansi udindo chifukwa zomwe zimachititsa kuti afune kutula pansi udindowu sizinachitike ndiye adakali wa pampando wa komitiyi,” anatsindika motere a Mwawa.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *