Anthu 7 amwalira pa ngozi ku Blantyre

Amayi asanu ndi awiri amwalira pa ngozi ya galimoto lolemba mu msewu wa Chileka m’boma la Blantyre.

M’neneri wa polisi ya Ndirande, a Maxwell Jailos, atsimikiza izi ponena kuti anthuwa amwalira atangofika nawo pa chipatala chachikulu cha Queen Elizabeth kaamba kovulala modetsa nkhawa kutsatira ngoziyi.

Galimoto yomwe yapanga ngoziyi, ndi lore ya mtundu wa Toyota Dyna (2 tonner) yomwe nambala yake ndi DZ 7873, ndipo pa nthawi ya ngoziyi inanyamula anthu okwana 37.

Anthu enanso kuphatikizapo dalayivala wa galimotoyi, a Davie Chingolo azaka 52, avulala pa ngoziyi.

Anthuwa amachokera ku bwalo la za masewero la Kamuzu komwe amakalandira chimanga cha ulere chomwe chikumaperekedwa ndi nthambi ya boma ya DoDMA.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *