Wachiwiri kwa mkulu wa apolisi Casper Chalera wamwalira

Wachiwiri kwa mkulu wa apolisi m’dziko muno Casper Chalera wamwalira.

M’neneri wa nthambiyi m’dziko muno, a Peter Kalaya, atsimikizira YFM online m’mawa uno kuti a Chalera amwalilira ku chipatala cha Kamuzu Central mu mzinda wa Lilongwe.

“Ndi zowonadi kuti amwalira dzulo usiku ku chipatala cha KCN ku Lilongwe komwe anatengeredwa,” atero a Kalaya mu uthenga omwe atilembera.

Malemu a Chalera amachokera m’mudzi mwa Matako mfumu yayikulu Lukwa m’boma la Kasungu.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *