Boma ladandaula ndi kuchepa kwa chidwi cha olemba ntchito

Unduna wa za umoyo wadandawula kaamba kakuchepa kwa chidwi chomwe anthu olemba anzawo ntchito akumayika pofuna kuti anthu awo adzikhala amaganizo angwiro.

Izi zanenedwa mu kalata yomwe yatulutsidwa ndi undunawu ndipo yasayinidwa ndi mlembi wake, Dr. Samson Mndolo.

Uthenga mu kalatayi ukudza pomwe dziko lino mogwirizana ndi mayiko pa dziko lapansi akhale akukumbukira za maganizo angwiro pa 10 October.

“Pamene anthu olemba anzawo ntchito akukonza nsanamira zothandizira kuti anthu awo adzikhala athanzi, palibe chidwi chenicheni chimene akuyika pankhani yokhudza kuthandiza maganizo angwiro,” yatero kalatayi.

Undunawu watinso kawirikawiri anthu ambiri ogwira ntchito samawulula za mavuto a m’malingaliro awo kamba koti amawopa kusalidwa choncho nkofunika kuti olemba ntchito anzawo ayike chidwi pa nkhaniyi.

Malingana ndi undunawu, pa dziko lapansi, munthu m’modzi mwa anthu asanu aliwonse amakhala ndi nthenda yokhudza m’maganizo.

Mwambo wa chaka chino ukukumbukiridwa pa mutu oti: “Nthawi yakwana yolabadira za maganizo angwiro kumalo ogwilira ntchito”.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *