Bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) latsutsa nkhawa za zipani zotsutsa m’dziko muno kuti bungweri liribe kuthekera koyendetsa chisankho cha chaka cha mawa.
Bungweri lanena izi kudzera mu kalata yomwe latulutsa kuyankhapo zomwe zidanena zipani za Democratic Progressive (DPP), UTM ndi Alliance for Democracy (AFORD) pa msonkhano wa atolankhani mu nzinda wa Lilongwe komwe zinati ziribe chikhulupiliro mwa bungweri komanso atsogoleri ake.
Mwa zina kalata ya MEC yatsutsa nkhawa za zipanizi zomwe zinati sizikukhutira ndi kampani ya Smartmatic yomwe bungweri linasankha kuti iziperekera zipangizo zogwiritsira ntchito pa chisankhochi kaamba koti kampaniyi iri ndi mbiri yolephera kugwira bwino ntchito m’mayiko ena.
Apa bungweri lati lisanapange mgwirizano ndi kampaniyi linachita kaye kafukufuku kuphatikizapo kupita ku ofesi za kampaniyi m’dziko la Taiwan kuyambira pa 28 January mpaka pa 2 February chaka chino.
Bungwe la MEC latinso linakafika m’mayiko a Zambia ndi Kenya komwe kampaniyi inagwirako ntchito yonga yomweyi ndipo bungweri linakhutira ndi ntchito za kampaniyi.
Pa pempho la zipanizi loti mkulu wa bungwe la MEC, Annabel Mtalimanja, achoke pa udindowu, kalatayi yati nthambi yowona za ku mabwalo a milandu ndi yomwe ili yoyenera kupanga chiganizo pa zakuthekera kwa wapampando wa bungweri kaamba koti ndi yomwe imasankha mayina a anthu oyenera pa udindowu asanavomerezedwe ndi mtsogoleri wa dziko lino pa udindowu.