Mtsogoleri wa chipani cha United Democratic Front (UDF), Atupele Muluzi, watsimikizira akuluakulu a chipanichi kuti palibe chipani chilichonse chomwe akukambirana nacho zopanga m’gwirizano pokonzekera chisankho cha chaka cha mawa.
A Muluzi anena izi lero mu nzinda wa Blantyre potsegulira mkumano omwe chipanichi chabweretsa pamodzi atsogoleri ake omwe anasankhidwa ku msonkhano wake wawukulu ndi cholinga chowapatsa upangiri pokonzekera kuyamba misonkhano ya chipanichi yokopa anthu kuti adzachivotere pa chisankho chikudzachi.
“Ngati pangakhale chipani chirichonse chomwe chingabwere nkundiwuza kuti chikufuna m’gwirizano, inuyo atsogoleri muzakhala oyamba kudziwa. Choncho pewani kumvera nkhambakamwa zomwe zikumangonenedwa m’matsamba a mchezo,” atero a Muluzi.
Iwo achenjezanso atsogoleriwa kuti omwe alephere kugwira ntchito yawo moyenera achotsedwa m’mawudindo.
“Maso a anthu ambiri ali pa chipani cha UDF pomwe chikukonzanso ntchito zake choncho tiyeni tiyiwale za m’mbuyo koma tipite chitsogolo ndipo ngati mukudziwa kuti simukwanitsa kugwira ntchito yomwe mwasankhidwira kulibwino mungotula pansi udindo,” anatsindika motero a Muluzi.
Ndipo m’mawu awo, wapampando wa chipanichi m’dziko muno a Lilian Patel, ati nthawi yakwana kuti chipanichi chiyambe kuchita zinthu zake mwatsopano potengeranso kuti dziko lapansi likusintha kayendedwe.