Nduna yowona za malimidwe a Sam Kawale yati boma ladzipereka pofuna kuthetsa njala mdziko muno pogwiritsa ntchito ulimi wothilira.
Iwo anena izi kwa mfumu Nkapita (Sub TA) m’boma la Zomba pa mwambo wa tsiku lokumbukira kufunika kokhala ndi chakudya chokwanira pa dziko lonse.
A Kawale ati ulimi wothilira ndi omwe ungathandize kwambiri kuti anthu azikhala ndi chakudya chokwanira pa khomo chaka chonse.
Iwo anati malo aakulu okwana mahekitala 3,700 m’boma la Zomba ndi omwe alimi akuchita ulimi wothirira wa m’ma sikimi ndipo anati undunawu uchita zothekera kuti ulimi wa mtunduwu uzichitika m’maboma onse.
Pa mwambowu, ndunayi inakhazikitsa ntchito yogawa chimanga ku maanja 75,344 a m’boma la Zomba omwe azilandira thumba limodzi lolemera makilogalamu makumi asanu (50) kwa miyezi isanu.