CDEDI yati ikukonza ziwonetsero zosakondwa ndi boma

Bungwe la Centre for Democracy and Economic Development Initiatives (CDEDI), lati lachinayi likudzali lichititsa ziwonetsero mu nzinda wa Lilongwe zosonyeza kukwiya ndi kupitilira kwakusowa kwa mafuta a galimoto m’dziko muno.

Malingana ndi kalata yomwe bungweri lalembera bwanankubwa wa khonsolo ya Lilongwe, cholinga cha ziwonetserozi ndikukakamiza nduna yowona mphamvu za magetsi a Ibrahim Matola komanso mkulu wa bungwe la MERA a Henry Kachaje kuti atule pansi ma udindo awo kaamba kolephera kuthana ndi vutoli.

Mkulu wa bungwe la CDEDI a Sylvester Namiwa, atinso adzagwiritsa ntchito ziwonetserozi pofuna kukakamiza bungwe la MEC kuti liyimitse kaye kalembera wa mukawundula wa mavoti yemwe ali mkati padakali pano kufikira bungweri litathetsa m’gwirizano wake ndi kampani ya Smartmatic yomwe ikuthandizira ntchitoyi.

Iwo ati kampani ya Smartmatic iribe kuthekera koyendetsa chisankho moyenera ndipo padakali pano iri mkati mofufuzidwa pankhani yomwe ikukhudzidwa ndi zachinyengo zomwe zinachitika m’dziko la Philippines.

Malingana ndi a Namiwa, ziwonetserozi zizayambira pa bwalo la Lilongwe Community ndikukathera pa chipata cha ofesi za boma ku Capital Hill komwe kukachitike m’bindikiro kufikira pomwe nkhawa za bungweri zitayankhidwa.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *