Chakwera walephera kulamulira dziko, watero Kabambe

Wolemba Lauryn M’banga

Mtsogoleri wa chipani cha UTM a Dalitso Kabambe, ati mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera alephera kulamulira dziko lino.

Poyankhula pa msonkhano wa atolankhani mu nzinda wa Lilongwe, a Kabambe anati uthenga wa a Chakwera ku mtundu wa Malawi lachitatu madzulo sunapereke chilimbikitso chilichonse pa nkhani yothana ndi mavuto omwe alipo m’dziko muno.

A Kabambe anadzudzula a Chakwera kamba kolephera kuchotsa ntchito mkulu wa bungwe la MERA a Henry Kachaje, nduna yowona za magetsi ndi mafuta a Ibrahim Matola pamodzinso ndi mkulu wa NOCMA.

Iwo anati a Chakwera amayeneranso kuchotsa ntchito nduna ya za ulimi a Sam Kawale kamba kolephera kuyendetsa bwino ndondomeko ya zipangizo za ulimi zotsika mtengo, komanso nduna ya zachuma a Simplex Chithyola Banda pamodzi ndi gavanala wa banki yaikulu ya Reserve a Wilson Banda kamba kolephera kuyendetsa bwino chuma cha dziko lino.

A Kabambe anatinso a Chakwera amayenera kuchotsa ntchito nduna yachitetezo a Ken Zikhale Ng’oma komanso mkulu wa apolisi a Merlyne Yolamu chifukwa cholephera kumanga anyamata onyamula zikwanje ndi zida zina zowopsa omwe akhala akuchitira uchigawenga anthu ochita ziwonetsero.

About Augustine Muwotcha

View all posts by Augustine Muwotcha →

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *