Bungwe la Center for Democracy and Economic Development Initiative (CDEDI) lati likufuna kuti zikalata za lipoti lokhudza za ngozi ya ndege yomwe inapha wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima ndi anthu ena asanu ndi atatu, ziperekedwe kwa a Malawi kuphatikizapo mabanja okhudzidwa.
Mkulu wa bungweri a Sylvester Namiwa, ndiwo anena izi pa msonkhano wa atolankhani mu mzinda wa Blantyre.
Iwo anena izi kutsatira zomwe ananena mtsogoleri wa komiti yomwe inakhazikitsidwa kuti ipange kafukufukuyu, a Jabbar Alide, yemwe anati zikalata za lipotiri, lomwe linawerengedwa loweruka lapitali, siziperekedwa kwa anthu koma m’malo mwake ziperekedwa kaye kwa mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera.
Malingana ndi a Namiwa, nkofunika kuti a Malawi aliwerenge lipotiri mwatsatanetsatane kaamba koti liri ndi zotsamwitsa zambiri zofunika mayankho.
Iwo atinso ali ndi umboni kuti mtsogoleri wa dziko linoyu anali atapatsidwa kale lipotiri lisanawerengedwe kwa mtundu wa a Malawi.
“Tinamva zija nzopanda pake, angotichedwetsa komanso kuwononga ndalama zathu,” atero a Namiwa.