Mlandu wa a Bushiri upitirira Lachitatu

Wolemba Emmanuel Yokonia

Woyimira anthu pa milandu, Wapona Kita, wati ndi wokhutira ndi m’mene ikuyendera ndondomeko yofunsa mafunso mboni ya boma a Sibongire Mnzinyathi pa pempho lofuna kutumiza mneneri Shepherd Bushiri pamodzi ndi mkazi wake, Mary mdziko la South Africa kuti akayankhe milandu.

A Bushiri ndi mkazi wawo, Mary akufunidwa ndi boma la South Africa kuti akayankhe milandu yochita zachinyengo komanso kuzembetsa ndalama pa nthawi yomwe adali akukhala mdzikolo asanabwerere ku Malawi.

Pomwe kumva mlanduwu kukupitirira mu mzinda wa Lilongwe, a Kita, omwe akutsogolera mbali ya ma loya a Bushiri, anawuza bwalo la milandu Lolemba kuti akwanitsa kuwonetsa mu bwalo kuti anthu awiriwo ndi wosalakwa.

A Kita anatsimikiza kuti zidzatengera mirakuli kuti a Bushiri ndi mkazi wawo adzatumizidwe ku South Africa chifukwa iwo awonetsa kuti milandu yomwe akuwaganizira awiriwa ilibe maziko oti atha kutumizidwa mdzikolo.

Mwa zina, a Kita anawonetsa kuti palibe ndalama zomwe a Bushiri anazembetsa kudzera ku makampani awo mosiyana ndi mmene lipoti la ofufuza za chuma a mdziko la South Africa.

Mkulu woyimira boma pa mlanduwu a Dzikondianthu Malunda anati ndi okondwa ndi momwe mboni ya boma yayankhira mafunso ochoka kwa woyimira a Bushiri ndipo ati mlanduwu ukuyenda momwe iwo amaganizira.

A Malunda anati mbali ya boma ndiyokonzeka kufunsa mafunso mboni yawo kuti idzalongosole bwino madera ena omwe siyinakwanitse kutero pa nthawi yomwe imafunsidwa ndi mbali ya a Bushiri.

Mulanduwu wayimitsidwa mpaka pa July 24, chaka chino.

About Augustine Muwotcha

View all posts by Augustine Muwotcha →

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *