Oweruza milandu wa bwalo la Chief Resident Magistrate ku Lilongwe a Madalitso Chimwaza wati adzapereka chigamulo mtsogolomu pa mlandu omwe boma la South Africa likufuna kuti mneneri Shepherd Bishiri pamodzi ndi mkazi wake, Mary akayankhe milandu yozembetsa ndalama, kuba ndinso kugwililira.
A Chimwaza alamula oyimira a Bushiri pa milanduyi kuti akhale atapereka kalata zawo zomaliza za mlanduwu pofika pa 19 August chaka chino.
Iwo alamulanso mbali ya boma kuti izakhale itapereka kalata zake zomaliza za mayankho pofika pa 13 September chaka chino.
Poyankhulapo mkulu woyimira boma pa mulanduwu a Dzikondianthu Malunda, anati mbali ya boma ndi yokhutira ndi momwe mulanduwu ukuyendera chifukwa choti tsogolo lake likuoneka.
A Malunda anati kalata zolembazi zipereka mwayi kwa woweruza milandu kuti awerenge bwino kalata za mbali zonse ziwiri.
M’modzi mwa omwe akuyimira a Bushiri pa mulanduwu a Wapona Kita anati mbali yawo ndiyokonzeka kupereka kalatazi pa 19 August chaka chino chifukwa omwe akuwayimilirawa akufuna milanduyi ithe mwa changu.