Nthambi yowona za ngozi zogwa mwadzidzidzi ya DoDMA yati ntchito zokonzanso zinthu zomwe zidawonongeka kaamba ka a namondwe, zikumachedwa kutha mwazina kaamba koti zipangizo zikuluzikulu zimafika mochedwa kuchokera mmaiko akunja.
Mkulu wa nthambiyi, a Charles Kalemba, wati dziko lino lingathane ndi mavutowa ngati lingalimbikitse kugwiritsa ntchito luso la ophunzira msukulu za ukachenjede ndi kampani za mdziko lino kuti zipangizozi, monga za ntchito yopopera madzi, zomwe zikugulidwa ku Germany ndi South Africa, zizitha kupangidwa m’dziko muno.
A Kalemba adandawulanso kuti kusamvana pa nkhani za malo komwe zitukukozi zikumangidwa kukumasokoneza ntchitozi choncho apempha ma bwanankubwa, mafumu ndi eni malowa kuti azikambirana modekha.
Iwo anena izi lachinayi nthambiyi itayendera ntchito zokonza malo ogawa madzi kwa anthu m’maboma a Zomba, Phalombe, ndi Mulanje omwe anawonongeka ndi a namondwe omwe akhala akukhudza dziko lino.
Ntchitoyi, yomwe ikugwiridwanso m’boma la Nsanje ndi ndalama pafupifupi $22 million zochokera ku Africa Development Bank (ADB), ndiyokhudza kupopa madzi ndikuwagawa kwa anthu pogwiritsa ntchito magetsi a dzuwa ndipo imayenera kutha mwezi wa July chaka chino.
A Kalemba komanso ma bwanankubwa ndi anthu m’madera omwe anayenderedwawa, ati ndiwokhutira ndi ukadawulo wa omwe akugwira ntchitoyi.
Komabe iwo adandawula ndikusapanganika kwawo pa nthawi yomwe amayenera kumaliza ntchitoyi yomwe tsopano alonjezedwa kuti itsirizidwa ndikuperekedwa m’manja mwa anthu mwezi wa mawa.