Wolemba Emmanuel Yokonia
Bungwe la National Youth Network on Climate Change lapempha boma kuti lisinthe malamulo omwe anakhazikitsidwa mchaka cha 1970 okhudza chitetedzo cha nyama ponena kuti mfundo zina zomwe zili mu malamulowa sizikugwirizana ndi mavuto omwe alipo panopa.
Poyankhula ndi YFM, mkulu wa bungweli a Dominic Nyasulu anati mwazina lamuloli silikambapo zokhudza mawetedwe aziweto ozilora kuti zizingoyenda osati kuzitsekera zomwe zimayika pachiopsezo moyo wa ziwetozi.
A Nyasulu, anapitilira kunena kuti kafukufuku yemwe iwo anapanga mchaka cha 2022 anapeza kuti kusasamalira ziweto kwabwino kumaikanso miyoyo pachiopsezo ya anthu omwe amadya ziwetozo.
Iwo anena izi mu mzinda wa Lilongwe pa maphunziro omwe bungweli linakonzera olemba nkhani okhudza chitetedzo cha ziweto.
Mmawu ake, katswiri za ziweto kuchokera ku sukulu ya ukachenjede ya LUANAR a Jonathan Tanganyika anati anthu omwe amaweta ziwetozi samadziwa bwino mmene angatetezere maufulu aziweto zawo.
A Tanganyika anati boma lithandize kufalitsa mauthenga kwa anthu mdziko muno makamaka omwe amaweta ziweto mmene angalemekezere ufulu wa ziweto.