Musalowetse ndale pa mapemphero, Arkiepiskopi Msusa achenjeza ansembe

Mtsogoleri wa mpingo wa Katolika mu Arkidayosizi ya Blantyre, Arkiepiskopi Thomas Msusa, achenjeza ansembe kuti asalore anthu a ndale kugwiritsa ntchito miyambo ya mapemphero pokopera anthu.

Dziko la Malawi chaka cha mawa lichititsa zisankho za makhansala, aphung akunyumba ya malamulo ndi mtsogoleri wa dziko.

Arkiepiskopi Msusa anati ansembe akuyenera kutengera chitsanzo chabwino cha yemwe anakhalapo mtsogoleri wa mpingo wa Katolika pa dziko lonse Papa Pius wa nambala 10 woyera yemwe anakanisitsa kugonjera atsogoleri a ndale kulowelera pa nkhani za mpingowu.

Iwo ayankhula izi Lamulungu ku Parishi ya St Pius ku Blantyre pa mwambo wa mapemphero omwenso unali wokondwerera nkhoswe ya parishiyi Papa Pius wa nambala 10 woyera.

Pa mwambowu, omwenso panali nthumwi zochokera ku mipingo monga Anglican ndi CCAP, Arkiepiskopi Msusa anaperekanso sacramenti la ulimbitso kwa a khirisitu ena omwe amapemphera pa kachisiyo.

Pa mapempherowa, mpingowu unachititsanso mwambo wogulitsa zinthu zosiyanasiyana pofuna kupeza ndalama zomangira kachisi watsopano ndi nyumba ya ansembe.

Bambo mfumu wa parishi ya St Pius, bambo John Chitsulo, anati ndalama zokwana K1.5 billion ndi zomwe zikufunika pa ntchitoyi.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *