Abambo atatu awamanga kamba kokupha m’bale wawo

Abambo atatu awamanga m’boma la Dowa powaganizira kuti apha mchimwene wawo Howard Yolamu pomubaya ndinso kumukhapa potsatira mkangano wokhudza malo a makolo awo.

A Joseph Yolamu ndi a Dick Nguluwe onse a zaka 48 pamodzi ndi a Peter Phesele a zaka 31, akuwaganizira kuti anabaya ndi mpeni komanso kukhapa a Howard Yolamu a zaka 53, ndi nkhwangwa, zikwanje ndi makasu.

Izi zidachitika pa nthawi yomwe iwo amalima m’munda wa pa mkanganowo pa 3 mwezi uno m’mudzi mwa Mphindu.

Mneneri wa m’boma la Dowa a Alice Sitima wati a Howard Yolamu anavulazidwa kwambiri ndipo anamwalira atangofika nawo pa chipatala cha Dowa.

About Augustine Muwotcha

View all posts by Augustine Muwotcha →

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *