Apolisi anjata bambo pomuganizira mulandu wogwilira

Bambo wa zaka 25, Clever Makina, ali m’manja mwa apolisi ku Blantyre pomuganizira kuti anagonana ndi msungwana wa zaka 16 komanso kumujambula kanema olawula ndikumuponya pa tsamba lake la mchezo.

M’neneri wa polisi ya Blantyre, Mary Chiponda, wati mai ake a msungwanayu ndiwo anakatula nkhaniyi ku polisi atawona kanemayu pa tsamba la mchezori ndipo atamufunsa mwanayo anawulula kuti Makina ndiye anamujambula kanemayu pomwe awiriwa anali limodzi mu chipinda chogona alendo ku Lunzu m’boma la Blantyre.

Mu August chaka chino, mkuluyu anayamba kucheza ndi msungwanayu kudzera pa tsamba la mchezo pomwe amagwiritsa ntchito dzina la chinyengo la munthu wa mkazi ndipo amamunamiza msungwanayu kuti amuthandiza ndi ndalama.

Kenaka mkuluyu anamunyengerera msungwanayu kuti akakumane ku Lunzu komwe anakamutengera m’chipinda chogona alendo komwenso anamujambula kanema olawula ndipo kenaka anamulamula kuti apereke ndalama zokwana K400, 000 kwinaku akumuwopseza kuti akapanda kutero atumiza kanemayu pa tsamba la mchezo.

Msungwanayu analephera kupereka ndalamayi ndipo mkuluyu anamuwuza kuti m’malo mwake angogonana naye zomwe msungwanayu anavomera pofuna kuziteteza, komabe ngakhale izi zinachitika mkuluyu anaponyabe kanemayu pa tsamba lake la mchezo.

Clever Makina ndi wochokera m’mudzi mwa Chimiko mfumu yayikulu Kapichi m’boma la Thyolo.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *