Wotayira mwana mchimbudzi agamulidwa miyezi 6

Wolemba Lauryn M’banga

Bwalo la milandu m’boma la Chikwawa lagamula kuti Maria Akimu wa zaka 20 akakhale kundende kwa miyezi isanu ndi umodzi chifukwa chotayira mwana wa khanda mchimbudzi.

Akimu anataya khandalo litangobadwa kumene, usiku wa pa 17 September chaka chino.

Pomwe anakawonkera ku bwalo la milandu loyamba la m’bomali, Akimu anavomera mlanduwu ndipo anapempha kuti amuchepetsere chilango, ponena kuti akufuna kubweleranso ku sukulu.

Oyimilira boma pa mlanduwu, a Amos Jobo anapempha bwaloli kuti lipereke chilango chokhwima, ponena kuti anapanga zinthu zosaonetsa umunthu komanso anayika moyo wa mwanayo pa chiopsezo.

Popereka chigamulo, woweruza milandu a Chiyembekezo Phiri anavomerezana ndi a Jobo, ponena kuti a Akimu anapalamula mlandu wawukulu komanso amadziwa zotsatira za zomwe amachitazo.

About Augustine Muwotcha

View all posts by Augustine Muwotcha →

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *