Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Dr Michael Usi, wanyamuka m’dziko muno lero ulendo wa ku Morocco komwe akakhale nawo pa msonkhano wa mayiko a m’bungwe la United Nations wokhudza nyanja zikuluzikulu.
Msonkhanowu wotchedwa United Nations Oceans Conference, uchitikira mu mzinda wa Tangier pa 9 October.
Nthumwi ku msonkhanowu zikakambirana mmene mayiko angakwaniritsire nsanamira ya maso mphenya achitukuko ya nambala 14 yomwe cholinga chake ndi kutetedza komanso kugwiritsa bwino ntchito nyanja zikuluzikulu komanso zachilengedwe zopezeka mnyanjazi.
Akachoka ku Morocco, a Usi akapitilira ku Azerbaijan komwe akakhale nawo pa msonkhano wokhudza zakusintha kwa nyengo omwe udzachitike pa 10 ndi pa 12 October.
Msonkhanowu cholinga chake ndikukonzekera mkumano wawukuluwu wa dziko lapansi wotchedwa COP29 womwe ukuyembekezeka kuchitika m’mwezi wa November.
Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko linoyu akuyembekezeka kubwerera kuno ku mudzi lolemba likudzali.