Bungwe la Centre for Democracy and Economic Initiatives (CDEDI) lapempha bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) kuti lisayambe gawo lachiwiri la kalembera wa anthu ofuna kuzaponya voti kufikira litathana ndi madando omwe aperekedwa.
Pempholi ladza pomwe zipani zotsutsa boma zikupitilira kusonyeza kusakhutira ndi m’mene bungwe la MEC likuyendetsera zokonzekera za chisankho cha patatu cha chaka cha mawa.
Mu kalata yomwe watulutsa, mkulu wa bungwe la CDEDI Sylvester Namiwa wati akugwirizana ndi pempho la zipanizi loti mkulu wa bungwe la MEC, a Annabel Mtalimanja, atule pansi udindo.
A Namiwa atinso akufuna kuti bungwe lazachisankholi lithetse mgwirizano wake ndi kampani yakunja ya Smartmatic yomwe ikuperekera zipangizo zoyendetsera chisankhochi.
Iwo achenjeza kuti ngati pemphori silimveka, bungwe la CDEDI silichitira mwina koma kuchititsa m’bindikiro omwe suzatha ku likulu la bungwe la MEC.
Bungwe la CDEDI latumiza kalatayi kwa mkulu wa bungwe la MEC komanso a kazembe a m’mayiko ena m’dziko muno.