Bungwe la National Youth Council of Malawi (NYCOM) lati zonse zokhudza mkumano wawukulu wa achinyamata mdziko muno omwe uyambe lolemba mpaka lachitatu sabata la mawa zili mchimake.
Mkulu wabungweri Rex Chipoka wauza atolankhani ku Lilongwe kum’mawaku kuti msonkhanowu omwe uchitikire ku BICC ukuyembekezera kukhala ndi mthumwi za achinyamata zoposera 500 kuchoka mbali zonse za dziko lino.
Pambali pa msonkhanowu, bungweri lidzakhalanso likukhazikitsa ndondomeko yammene agwilire ntchito mu zaka zisanu kuchokera chaka chino mpaka mchaka cha 2025.
“Inu mukudziwa kuti dziko lino chiwelengero cha anthu ambiri ndi achinyamata. 80 mwa anthu 100 aliwonse ndi achinyamata komanso ana omwe ndi azaka zochepera 35 kotero mkumano uwu ndi ofunika kwambiri kuti achinyamata apereke mfundo zawo za mmene tingapititsire patsogolo dziko lino.
“Achinyamatawa adzakambirananso mfundo zomwe zinthandizire dziko lino kukwaniritsa masomphenya a Malawi 2063 monga mukudziwa kuti achinyamata ali pa tsogolo pa masomphenyawa,” atero a Chipoka.
Pa mkumanowu achinyamata, akulu akulu aboma ndi atsogoleri a mabungwe akuyembekezerekanso kudzagundana mitu pa nkhani yokhudza kusowa kwa ntchito, gawo la achinyamata pa chisankho cha chaka cha mawa mwa zina.
Bungwe la NYCOM likhalanso ndi msonkhano wake wapa chaka (General Assembly) omwe wakhala usakuchitika kwa zaka zisanu ndi zitatu kamba kosowa ndalama.
Mutu wa msonkhanowu ndi ‘Kubweretsa mphamvu zatsopano zomwe achinyamata angatenge pofuna kukwaniritsa masomphenya a Malawi 2063’.