Nthambi ya ndende ilimbikitsa ntchito za luso la manja

Nthambi ya ndende m’dziko muno yati kuphunzitsa anthu omwe akugwira ukaidi luso la ntchito za manja ndi njira imodzi yomwe ingathandize kuchepetsa vuto la kuthinana ndi mchitidwe wa ukabwerebwere.

Mkulu wa nthambiyi, a Masauko Wiscot, anena izi loweruka ku ndende ya Zomba pa mwambo wopereka ma satifiketi kwa akaidi 48 omwe amaliza maphunziro awo a luso la ntchito za manja monga kusoka zovala mwazina.

Poyankhula ndi YFM online, a Wiscot ati kuphunzitsa akayidi lusoli ndikothandiza kuti akhale anthu osinthika ndipo akathe kudziyimira pawokha akabwerera kumidzi kwawo.

Ndipo kumbali yake, mkulu wa bungwe la Center for Human Rights Education, Advice and Assistance (CHREAA), a Victor Mhango, apempha ndi kulimbikitsa akayidiwa kuti akatuluka kundende akathe kugwiritsa bwino ntchito luso ndi upangiri womwe apeza kuti akathe kutukula miyoyo yawo.

Mkulu woyimilira bungwe la DVV International, lomwe limapereka ndalama zothandizira ndondomeko yophunzitsa akayidiwa, a Gerhad Quincke, ati ndiwokondwa kuti akayidiwa amaliza maphunziro ndipo bungwe lawo lipitilila kuthandiza nthambi ya ndende m’magawo osiyanasiyana.

Bungwe la CHREAA lakhala likugwira ntchito yophunzitsa akayidi luso la ntchito za manja monga kusoka, ukalipentala, kumeta tsitsi komanso zowotcherera kudzera ku thandizo la ndalama zochoka ku bungwe la DVV International.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *