CSAT yati iyamba kuphunzitsa anthu zokhudza nyumba ya malamulo

Bungwe la Centre for Social Accountability & Transparency (CSAT) lati kuyambira mwezi wa January chaka cha mawa lilimbikitsa ntchito yodziwitsa nzika za dziko lino za kagwiridwe ntchito ka nyumba ya malamulo komanso udindo wa aphungu m’nyumbayi.

M’modzi mwa akuluakulu ku bungwe la CSAT a Moffat Phiri anati cholinga cha ntchitoyi ndikuna kuti isanafike nthawi yoponya voti, nzika zidzakhale ndi chithunzithunzi choyenera cha nyumba ya malamulo yokhala ndi aphungu omwe adzakhale ndikuthekera kothandiza pa chitukuko cha dziko lino.

“Tikufuna kudzafunsa nzika za dziko lino kuti Kodi nyumba ya malamulo imene akuyifuna chikatha chisankho izakhale yotani? Izidzagwira ntchito motani? Nanga ntchito zake zidzakwaniritsidwe motani?” atero a Phiri.

Iwo anena izi mu nzinda wa Blantyre pa mkumano omwe bungwe lawo linasonkhanitsa pamodzi atolankhani ochokera nyumba zofalitsa nkhani za m’madera.

Cholinga cha mkumanowu chinali kuwadziwitsa za ndondomeko ya bungweri yomwe cholinga chake ndikulimbikitsa ulamuliro wabwino wa demokalase m’dziko muno pothandizira ntchito za kayendetsedwe ka nyumba ya malamulo.

Atolankhaniwa anapatsidwanso upangiri pa momwe angagwiritsire ntchito lamulo la kapezedwe ka nkhani mosavuta polemba nkhani zochitika ku nyumba ya malamulo.

About Augustine Muwotcha

View all posts by Augustine Muwotcha →

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *