Mtsogoleri wa chipani cha Democratic Progressive (DPP) a Peter Mutharika ati ndi wokwiya ndi kumangidwa kwa posachedwapa kwa akuluakulu a chipanichi.
“Ndiri ndi chisoni komanso okwiya kwambiri chifukwa anthu akumangidwa popanda chifukwa.
“Ndikupempha abusa a Chakwera kuti boma lanu lisiye nkhaza pozunza a Malawi komanso DPP ndipo m’malo mwake mulimbane ndi njala ndi umphawi m’dziko muno,” atero a Mutharika.
A Mutharika alankhula izi lero kwa Luwanda ku Machinjiri ku Blantyre komwe akuchititsa misokhano yoimaima.
Akuluakulu a chipani cha DPP motsogozedwa ndi a Mutharika, akonza ulendo oyendera anthu m’madera angapo munzinda wa Blantyre kuphatikizapo madera a Mbayani, Chemusa, Ndirande ndi Bangwe.