Anthu ena ku Balaka akufuna bwanamkubwa achoke

Mzika zokhudzidwa zochokera m’mudzi mwa Ng’onga mfumu yayikulu Nsamala m’boma la Balaka, zakonza ziwonetsero za bata zomwe cholinga chake ndikukakamiza unduna wa maboma aang’ono kuti usamutse bwanankubwa wa bomali, a Tamanya Harawa.

Kalata yomwe yasayinidwa ndi nthumwi za nzikazi, kupita kwa mlembi mu unduna wa maboma ang’ono, ku polisi komanso ku ofesi ya bwanankubwayu, yati ziwonetserozi zichitika lachinayi likudzali.

Anthuwa ati ndiwokhumudwa ndi bwanankubwayu kaamba koti akumuganizira kuti ndiye gwero lomwe likupangitsa kuti madandawulo awo okhudza kutengeredwa mwa chinyengo kwa malo awo ndi kampani yopanga simenti ya Potland aponderezedwe.

Mkwiyo wa anthuwa pa nkhaniyi yomwe inayamba pa kanthawi, wakulanso kutsatira zomwe anachita bwanankubwayu pa 3 February chaka chino pomwe anakana kulandira kalata yawo ya madandawulo okhudza nkhani ya malowa.

“Popeza amayenera kulandira kalata ya madando ndi DC malinga ndi malamulo, patsikuli sitikapereka petition. Kuyenda kwathu ndiye petition yathu. Izi zili chonchi chifukwa choti a DC anakana kulandira kalata yathu lolemba pa 3 February 2025,” yatero kalatayi.

Gwero la nkhaniyi ndilakuti anthuwa akhala akundawula kuti kampani ya Potland yomwe ndi ya mdziko la China inatenga malo awo ndikukhazikitsako ntchito zake zopanga simenti koma ndondomeko yomwe inatsatidwa sinakomere anthuwa kuphatikizapo kuti panachitika za chinyengo pa chipepeso chomwe ena okhudzidwa anapatsidwa.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *