Mavuto a zachuma akuchititsa anthu kuyika miyoyo yawo pa chiswe

Mavuto a zachuma akupangitsa anthu ochuluka kuyika miyoyo yawo pa chiswe pomwe akumalora kugwira nyansi ndi manja awo pofuna kupeza zinthu monga mabotolo a pulasitiki ndi zina kuti akagulitse.

Anthuwa amalawira m’mawa kuyendera m’mazala komanso ma bini momwe amapezamo katunduyu.

Zaka pafupifupi zisanu zapitazi, a Martin Tsamba azaka 62 omwe akukhala ku Mbayani mu mzinda wa Blantyre, anachoka kumudzi kwawo ku Chikwawa m’mudzi mwa Ntondeza mfumu yayikulu Maseya ndi cholinga chozayesa kupeza ntchito zoti ziwapezese ndalama.

Pochoka ku mudzi kwawo, a Tsamba anasiya mkazi ndi ana anayi ndipo anali ndi chiyembekezo choti m’tawuni azapeza chochita kuti pamapeto pake azithandiza banja lawo ku mudzi koma izi sizinathekhe.

Iwo m’malo mwake anangoyamba yofukula m’malo otayira zinyalala momwe amafukulamo zinthu monga mabotolo omwe amakagulitsa mu msika wa Blantyre pa mtengo wa K25 limodzi.

YFM online inachezanso ndi Godson Chigalu wa zaka 17 yemwenso ntchito yake ndi yomweyi.

Mnyamatayu akuti anayamba ntchitoyi kaamba ka umphawi omwe ankakumana nawo kwawo komwe iye pamodzi ndi abale ake amakhala ndi mai awo kamba koti bambo awo anachoka kalekale banja litatha.

Godson anasiya sukulu ali mu sitandade 5 pa sukulu ya pulayimale ya Mbayani kaamba kosowa thandizo.

Kupatula kutola zinthu zomwe amakagulitsazi, anthuwa amapezeraponso mwayi otola zakudya zomwe zimatayidwa m’malowa ndikumapulumukirapo.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *